Chisamaliro cha a bambo (Chechewa)

Khistofa Makawa
Khistofa Makawa

Bambo ake a Khristofa Makawa anasautsidwa kwambiri ndi khalidwe la mwana wawo, ndipo tsiku lina anakhala naye pansi kuti amudzudzule pa za moyo wake. Bambo ake anali mtumiki mu mpingo wa Christian Brethren ndipo ankadziwa *choona cha uthenga wabwino okhudza chikhululukiro chopezeka mwa Yesu Khristu. Ankafuna kuti Khristofa adziwe za chikhululukiro chimenechi.

Monga mnyamata Khristofa ankayambitsa mabvuto pakati pa anzake, ankakonda kuwamenya ngakhalenso kuwabera. Kenako anayamba kukhala moyo wosayenera ndipo ankalephera kugwiritsa bwino ntchito ndalama zomwe zotsatira zake anali mabvuto a ngongole. Moyo wake unatayika, ndipo ankalephera kudzithandiza kuti asiye machimo omwe anawazolowera.

Khristofa analibe nthawi ya zinthu za uzimu. Iye amakumbukira, "Ndinkaganiza za Mulungu chifukwa ndinabadwira m'banja la chiKhristu, ndipo makolo anga ankakonda kumanditengera ku tchalitchi kukapemphera la Mulungu."

Baibulo limanenetsa kuti kukhala ndi makolo omwe amakhulupirira mwa Mulungu sikupanga mwana wawo kukhala wabwino pa maso pa Mulungu. 'Onse anachimwa naperewera pa ulemerero wa Mulungu,' Aroma 3:23 mau amatero.

Khristofa anayamba kusautsidwa ndi khalidwe lake, ndipo anapezeka kuperewera. "Ndinatayika," Iye amanena.

Pofotokoza kwa Khristofa chomwe chinalakwika m'moyo wake, bambo ake anatsekula Baibulo lawo madzulo amenewo m'kalata yoyamba ya Yohane, Mutu 3 ndime ya 8, yomwe imati, 'Yense wakuchita tchimo ali wa Satana, pakuti Satana ndi wochimwa kuyambira pa chiyambi. Chifukwa chimene Mwana wa Mulungu anadzera ndi kuzawononga ntchito za Satana.'

Khristofa akufotokoza chomwe chinachitika atazindikira choona chomwe ndimeyi inamuuza, "Nditamva uthengawu ndinatsutsika za moyo wanga (za kuchita zoipa), ndipo ndinalapa machimo anga ndikumupempha Mulungu kuti andikhululukire. Pambuyo pake ndinamupempha Ambuye Yesu kuti alowe mu mtima mwanga."

"Ndinamva za Uthenga Wabwino (uthenga wa chikhululukiro cha tchimo) kunyumba kwathu madzulo amenewo, pomwe bambo anga analalikira ku banja lathu," Khristofa amakumbukira. Bambo ake anali ndi chizolowezi chowerenga Baibulo ndi kupemphera tsiku ndi tsiku ndi banja lawo akamaliza kudya mgonero m'nyumba mwawo.

"Ndinazindikira tchimo langa ndipo mwachangu ndinadziwa kuti Yesu Khristu anafera pa mtanda kaamba ka machimo anga kuti ndikhale ndi moyo." Iye akupitiriza, "Kutsatira Satana umakhala kapolo ku tchimo ndipo sungakondweretse Mulungu. Ndinasankha kukhala Mkristu chifukwa muli moyo wosatha (Moyo weniweni wa uzimu) ndi kupembedza komwe ndi koona."

Kodi Khristofa Makawa ali ndi chitsimikizo chanji kuti ali bwino pamaso pa Mulungu Woyera?

Akufotokoza momwe anaonera moyo wake ukusintha, china chomwe chomwe sankakwanitsa kuchita ndi mphamvu zake payekha asanakhulupirire mwa Yesu Khristu.

"Ndinangomupempha Mulungu kuyamba kulamulira moyo wanga," akutiuza. "Posakhalitsa zitatha izo ndinayamba kukonda adani anga, ndipo ngongole zonse zomwe ndinali ndisanalipire—ndinayamba kubweza. Ndinawathandiza makolo anga mu ntchito zambiri."

Ichi chinandipangitsa kuzindikira kuti ndine Mkristu (woona) chifukwa moyo wanga unasinthiratu!"

Umboni wina wakuti chipulumutso cha machimo ake chinasintha moyo wake ndi chakuti, pano ali ndi chidwi chachikulu kuwauza ena mosaopa zokhudza chikhululukiro chodabwitsa chopezeka mwa Yesu Kristu.

Anthu ena anampempha Khristofa kusiya mpingo wake ndi kuti akalowe mpingo wawo, anamuyesa pa kumpatsa galimoto ngati akanatha kuwatsatira. Komabe, chuma ndi zinthu si kanthu konse kuyerekeza ndi mtendere uli mwa Yesu Kristu. Mwanzeru anasankha kuti sakodwe m'msampha womwe mdani Satana Mdyerekezi anamutchera.

Iye akuti, "Ndime yomwe yandithandiza kwambiri ndi Aefeso 5:15 yomwe imati, 'Samalirani bwino mayendedwe anu. Musayende ngati opanda nzeru, koma monga anzeru.'"

"Pangani chisankho cha kumulandira Yesu Khristu lero lino, chifukwa tikakhala m'mabvuto Yesu samathawa, Amapereka mtendere! Satana amangobwera pa moyo wathu kwa nthawi yochepa ndipo tikazingwa amatithawa," akutsiriza motere Khristofa.

Chinali cha nzeru motani kuti bambo ake a Khristofa agawane chikhulupiriro chawo mwa Mulungu ndi mwana wawo; zinasintha moyo wake kwa muyaya. Bambo ali ndi udindo waukulu pamaso pa Mulungu pa kutengera ana awo ku ulemerero wa Mulungu.

<< A father’s care
Soldier finds life as he faces death >>